03/09/2026
Msonkhano wa Ukaristia womwe ukuchitika m'dayosizi za Mpingo wa Katolika m'dziko lino, lero uli ku St. Augustine Cathedral m'dayosizi ya Mangochi.
Bishop Montfort Stima wa dayosiziyi ndiye akuyembekezeka kutsogolera msonkhanowu womwe udzathe Loweruka, ndipo Akhristu, ansembe ndi asistere a parishi zosiyanasiyana za dayosiziyi akhala akutenga nawo mbali.
Uwu ndi msonkhano wapaderadera wa Mpingo onse mu dayosiziyi womwe cholinga chake ndi kumvetsera, kulemekeza ndi kuyanjananso ndi Mwini wake wa Ukaristia, Yesu Khristu, ndipo ukutsatira msonkhano wa dziko lonse womwe unachitika chaka chatha ku Lilongwe.
Ansembe, asisteri, abulazala ndi Akhristu eni ake afika ku msonkhanowu, womwenso ukuchitika m'dayosizi za Zomba ndi Chikwawa.
Pakadali pano, mwambo wa (wopembedza) Ukaristia womwe akutsogolera ndi Bambo David Mambo uli mkati pa Mangochi Cathedral.