05/01/2026
CHENJEZO LA MVULA YAMPHAMVU YOMWE INGAPANGITSE MADZI KUSEFUKIRA KUYAMBIRA PA LACHITATU PA 07 JANUARY 2026 MPAKA LACHISANU PA 09 JANUARY 2026
Nthambi yoona Zanyengo ndi Kusintha kwa Nyengo ikupereka chenjezo lokhudza mvula yamphamvu yomwe ikuyembekezereka kugwa ndipo kukhoza kupangitsa madzi kusefukira. M’madera ena mvulayi idzabwera mophatikizana ndi mphepo yamkuntho komanso yamabingu. Izi ndi kamba ka dera lopepuka lomwe likuyembekezeleka kukhazikika pa Malawi ndipo ikhala ikulimbikitsa mphepo za Congo pa Malawi lachitatu.
Madera omwe akuyembekezereka kukhuzika ndi Nkhotakota, Salima ndi madera ena aku Mzimba, Kasungu, Nkhata Bay, Dowa, Mchinji ndi Ntchisi, ali mu category 10, Mzuzu, Likoma, Machinga, Mangochi ndi madera ena aku Zomba ndi Balaka ali mu category 6, komanso madera ena ambiri ndi omwe ali mu category 5.
Nthambiyi ikudziwitsanso a Malawi kuti Namondwe otchedwa GRANT yemwe anabadwira mbali za ku Australia tsopano ali mu Indian Ocean koma wafooka ndipo alibe chiopsezo ku dziko la Malawi.
© Department of Climate Change and Meteorological Services