12/02/2026
Tsiku Limene Tinaika M’manda Munthu Wamoyo
Gawo 1
Sindinalire pa mwambo wamaliro.
Anthu onse ankayembekezera kuti ndilire—chifukwa James ndi ine tinakulira limodzi.
Tinkathamangitsa mbuzi m’mphepete mwa nyanja, tinkaba mango m’mitengo ya anthu ena, ndipo tinkalota maloto ang’onoang’ono ngati mmene achinyamata amachitira moyo ukuwoneka kutali.
Munthu akamwalira, umayenera kulira.
Makamaka akakhaka wamwalirayo ndi wachichepere komanso akakhala kuti anali nzako.
Koma pamene ankatsitsa thupi lake m’manda, chimene ndimamva sichinali chisoni…
Chinali chisokonezo. Chifukwa James samawoneka ngati munthu wakufa.
Nkhope yake inali bata kwambiri, ngati munthu amene wangogona chifukwa chakutopa ndi ulendo wautali. Anamwalira osadwala.
Anangomukulunga m’mphatsa yolimba, kungobisa chifuwa chake, manja ake, mapazi ake. Adzukulu ankagwira ntchito mofulumira.
Mofulumira kwambiri. Panalibe bokosi la maliro. Mphatsa yokha. Panalibe mapepala ochokera kuchipatala osonyeza kuti munthu wamwaliradi.
Ndipo abale ake ochokera kutali sanadikiridwe kuti afike. Samalora munthu kufunsa mafunso.
Nditafunsa mmodzi mwa akuluakulu akubanja chifukwa chimene sitinamutengere James kuchipatala, sanandiyang’ane n'komwe.
Maso awo anangoyang'ana pansi. “Pali Imfa zina,” anatero mwakachetechete, “siziyenera kukhala Nthawi yaitali munthuyo asanaikidwe.”
Mayi wina pafupi nane anangopinda miyendo. Ndipo Wina anatchura dzina langa mwachangu, kundichenjeza kuti ndikhale chete, ndisalankhule ngati ndisakufuna mavuto.
Ndinameza mawu anga. Ndinachita mantha m'malo mwake. Ndipo nyimbo zinayamba—pang’onopang’ono, mosalekeza—zolimbikitsa amoyo, zosokoneza akufa (kwathu sipadziko tingopitilira).
Fumbi linakwera mumlengalenga pamene anthu ankayenda mwachisoni. Dzuwa linali likutentha.
Kenako ndinazizidwa ndi mantha ankulu.
Pamene donthi loyamba linagunda thupi la James… Zala zake zinasutha.
Kamodzi kokha.
Kugwedezeka kochepa.
Mpweya unandithera m’khosi. Ndinatsegula pakamwa panga kuti ndifuule, kuti a