18/08/2023
Timu ya FCB Nyasa Big Bullets yafika mu mzinda wa Malabo ku Equatorial Guinea komwe ikuyembekezeka kusewera masewero ake ndi Dragon FC mu mpikisano wa CAF Champions league.
Oyendetsa ntchito za timuyi a Albert Chigoga wauza Zodiak kuti palibe chotsamwitsa chili chonse ndipo timuyi yakonzeka kusewera masewero ake oyamba mu mpikisanowu lamulungu lino.
Malinga ndi a Chigoga chiyembekezo chilipo kuti ulendo uno timuyi siyitulukira mu ndime ya chipulula ngati mene zakhala zikuyendera zaka za m'mbuyomu.
(by Dickson Chivwati Gondwe-Lilongwe:08/18/23)