16/03/2026
🇲🇼
Aphungu a nyumba ya malamulo ayambiranso zokambirana zawo zandondomeko yachuma ya 2026/27, zokambiranazi zitaima kwa sabata ziwiri pomwe makomiti anyumbayi amaunikira ndondomeko yachuma yomwe nduna ya zachuma a Joseph Mwanamvekha anapereka ya ndalama zokwana K10.978 trillion.
Sipikala wa nyumbayi, a Sameer Suleman, wauza aphungu kuti mtsutso wa ndondomeko yachuma uchitika kwa masiku asanu, kuchokera lero Lolemba.
Mkulu wa aphungu ambali yotsutsa a Simplex Chithyola Banda, ati ndi zofunika kuti maina a anthu omwe akutchulidwa mu kafukufuku wa malonda a hotela ya Amaryllis ndi thumba loona zandalama za pension za ogwira ntchito m'boma, kuti ayambe aima kaye pantchito.
Koma phungu wa dera la Dedza Kasina, a Joshua Malango, wapempha sipikalayu kuti achitepo kanthu pa chitetezo cha mamembala a komiti yomwe ikufufuza nkhani ya malonda a hotelayi, ponena kuti akuopsezedwa ndi anthu ena.
Poyankhapo, a Suleman ati ofesi yawo ikudziwa zankhanizi ndipo ikulumikizana ndi komiti ya Public Accounts Committee pa zonse zofunikira.
Wolemba; UKATIULODZWE PHIRI