Classic Embroidery

Classic Embroidery Contact information, map and directions, contact form, opening hours, services, ratings, photos, videos and announcements from Classic Embroidery, Screen Printing & Embroidery, Blantyre.

Coming soon
08/08/2025

Coming soon

GOAL LINE - KNOW YOUR CAST:

Katswiri wa lero ndi Blessings Suya. Uyu ndi m'modzi mwa akatswiri amene atengapo mbali mu Goal Line. Iyeyu watenga gawo ngati Chaponda Ntumwi amene ndi mphunzitsi mu kanemayu.

Blessings wakhala akupanga zisudzo kuyambira m'chaka cha 2004 ndipo watenga mbali zosiyanasiyana. Iyeyu wapanga ma sewero a pa wailesi monga Theatre of the Air komanso Stories in Action. Watengaponso mbali mu Choices pa MBC TV, Mitekete pa Times ndi ena. Alinso mu ma filimu monga All We Have Is Us ndi The Road to Sunrise.

Blessings wati ali ndi chikhulupiliro ndi tsogolo la ntchito za luso ku Malawi kuno ndipo wapempha boma kuti lipitilize kutengapo mbali mu ntchito zotukula ntchito za luso. Iye wati Malawi ali ndi kuthekera kopita pa mwamba mu ntchito zimenezi.

Blessings Suya amene amachokera ku Lunzu, kwa mfumu yaikulu Kapeni m'boma la Blantyre wati amakonda kudya chakudya chathu cha chi Malawi monga mpunga, nyemba, nyama ya mbuzi ndi therere.

Katswiriyu wati amakonda Denzel Washington ngati katswiri wa zisudzo za pa kanema.

Kanema wa Goal Line wajambulidwa ndi thandizo lochokera ku Macra kudzera ku bungwe lotchedwa Universal Service Fund ( USF).

Coming soon
07/08/2025

Coming soon

GOAL LINE - KNOW YOUR CAST:

Leronso tabwera ndi katswiri wina amene watenga mbali yaikulu mu kanema wa Goal Line. Iyeyu dzina lake ndi Chifundo Sumani ndipo akutenga mbali ngati Tryphina Bashir.

Chifundo ndi msungwana wa luso kwambiri pa zisudzo ndipo wakhala akupanga izi mwa ka nthawi ndithu. Pambali pa luso limeneli, Chifundo ndi katswiri osewera mpira wa miyendo wa atsikana ndipo wakhala akusewera mu ma timu monga; Kamuzu Barracks, Chilinde Women's, Blue Eagles, Bangwe All Stars ndi Ekhaya.

Iyeyu wati amakonda Make Sikono ngati katswiri opanga zisudzo za kanema m'dziko lino.

Pambali pa izi, Chifundo amene amachokera ku Machinjiri m'boma la Blantyre, ali ndi Bachelor's degree in Applied Accounting, Auditing and Information Systems.

Kanema wa Goal Line wajambulidwa ndi thandizo lochokera ku Macra kudzera ku bungwe lotchedwa Universal Service Fund ( USF).

Coming soon.
06/08/2025

Coming soon.

GOAL LINE - KNOW YOUR CAST:

DEUS SANDRAM aka BWANDE

Lero tabwera ndi katswiri amene ndi m'modzi mwa anthu odziwika bwino m'dziko lino chifukwa cha luso ndi ukadaulo wao pa ntchito zambiri, makamaka, zoulutsa mau. Awa ndi a Deus Sandram omwe amadziwikanso ndi dzina loti Obwande pa wailesi. Iwowa atenga mbali ngati Bashir mu kanema wa Goal Line.

A Sandram ndi mkhala kale pa zisudzo ndipo akhala akupanga izi pa stage, pa wailesi komanso ngakhale pa kanema. Katswiriyu wakhala akutengapo mbali mu ma sewero a pa kanema monga, Tikuferanji, Choices komanso Mitekete mwa ena. Mkuluyu wapangaponso nawo ma filimu a pamwamba monga, Living on Perfume, All We Have Is Us, The Road to Sunrise ndi ena ambiri. Pambali pa izi, a Sandram amatenganso nawo mbali mu ma sewero a pa wailesi monga Theatre of The Air ndi Stories in Action pa MBC Radio.

Katswiriyu wati amagwiranso ntchito ngati mtolankhani ndipo program yao ya BWANDE yakhala ikuulutsidwa kwa zaka 21 tsopano. Pakadali pano, Sandram ndi wapampando wa Board ya alakatuli m'dziko lino yotchedwa Poetry Association of Malawi. Iyeyu wati amaongoleranso miyambo yosiyanasiyana( Director of Ceremonies). Pamwamba pa izi, Deus Sandram akupikisana nawo pa zisankho za phungu wa nyumba ya malamulo( MP) wa dera la South Lunzu Constituency mu mzinda wa Blantyre.

Iyeyu wati amatayira kamtengo malemu Hope Chisanu komanso malemu Samuel Kuseka ngati akatswiri a zisudzo m'dziko lino.

Kanema wa Goal Line wajambulidwa ndi thandizo lochokera ku Macra kudzera ku bungwe lotchedwa Universal Service Fund ( USF).

08/06/2024
Visit us today at Stand No. 5H, Chichiri Tradefair Grounds, Blantyre. For in-house digitizing and embroidery at affordab...
22/06/2023

Visit us today at Stand No. 5H, Chichiri Tradefair Grounds, Blantyre. For in-house digitizing and embroidery at affordable prices.

16/09/2020
New designs celebrating the inauguration ceremony and Independence Day.
02/07/2020

New designs celebrating the inauguration ceremony and Independence Day.

Beautiful artworks and designs done in-house!Visit us today and appreciate what has cemented our name as pioneers of emb...
28/05/2020

Beautiful artworks and designs done in-house!Visit us today and appreciate what has cemented our name as pioneers of embroidery in Malawi.

Beautiful artworks done in the house, New logo digitising done within hours.Visit us!!Stand number 5H, Chichiri Trade fa...
01/12/2018

Beautiful artworks done in the house,
New logo digitising done within hours.
Visit us!!
Stand number 5H, Chichiri Trade fair grounds, Blantyre.

Beautiful artworks done in the house!
27/09/2018

Beautiful artworks done in the house!

Address

Blantyre

Telephone

+265993910268

Website

Alerts

Be the first to know and let us send you an email when Classic Embroidery posts news and promotions. Your email address will not be used for any other purpose, and you can unsubscribe at any time.

Share