26/08/2026
Asilikari andende mdziko muno akwanitsa kulanda lamya zammanja 500, ma simukadi 1,000, ma kilogalamu asanu a chamba, ndi katundu wina oletsedwa mu ndende yaikulu ya Zomba Maximum.
Izi ndimalingana ndi ukadawulo wawo owonetsetsa kuti zipangizo zoletsedwa zisamapezeke ndi akaidi mu ndende zadziko muno.
Mneneri wandende mdziko muno,Steve Charles Meke ndiye wasimikiza izi ndi wailesi ya Kuwala Fm.
Image source:Social media