10/10/2025
"Kudzakhala kulandira mphoto zosiyana siyana tsiku lokumbukira anakubala kwa anthu amene adzakhale nawo pa majowajowa omwe takonza. ” — Mohammed Ajussah
Mkulu wa Emcee Gym n Fitness Center ku Mangochi, Mohammed Ajussah, watsimikiza kuti anthu adzakhala akupatsidwa mphoto, monga zipewa, ma T - Shirt, komanso ena adzatha kupeza mwayi ochita masewero olimbitsa thupi, ku Emcee Gym mwa ulele kwa mwezi umodzi pa tsiku losangalala anakubala, 15 October, mwezi uno.
Poyankhula ndi Blantyre Broadcasting Channel; Ajussah wati tsikuli lidzakhala la mtengo wapatali, ndipo kudzakhala masewero osiyana siyana monga, mpikisano wodumpha mumasaka, pachingirezi sack race, kupimana mphavu kukokerana chingwe, (tug of war), komanso majowajowa mwa zina.
Zonsezi zidzachitikira pa Mangochi Municipal Hall car park, ndipo ofuna kutenga nawo mbali, adzalipira MK 3000 akulu ndipo ana MK 2000 yokha basi.
Iwo akumema anthu okhala ku Mangochi kuti adzafike mwa unyinji, kudzasangalala limodzi ndi anakubala komanso kupha mbalame ziwiri ndi mwala umodzi.
Wolemba: Henry Ntontholi
Blantyre Broadcasting Channel Updates
93 Blantyre Fitness Magazine