Matindi JourNey

Matindi JourNey Contact information, map and directions, contact form, opening hours, services, ratings, photos, videos and announcements from Matindi JourNey, Marketing Agency, Lilongwe.

Lero ndi sunday tikapempheleko pilizi kapena tizichita kugendana mpaka kuti mupiteko ku church zoona
15/09/2024

Lero ndi sunday tikapempheleko pilizi kapena tizichita kugendana mpaka kuti mupiteko ku church zoona

Mukhoza kutitukwana koma dont forget to like and follow our page akumudzi.
08/09/2024

Mukhoza kutitukwana koma dont forget to like and follow our page akumudzi.

08/09/2024

Kumapemphela guyz masikuwa akuthamanga.
Yelemiya 22 v 10
musamlirire wakufa,musachite maliro ache;koma mumliritse iye amene amuka,pakuti sadzabwelelaso,kapena kuonanso dziko lakwao.

07/09/2024

Tigaweko airtime koma tsiku lina pamudzi pano

20/01/2024

ZOMWE ZINGATHANDIZE KUTI MWANA AZICHITA BWINO KU SUKULU

Makolo ambiri amafooka mwana wawo akamalakwa mkalasi ndipo ndavapo ambiri akumangoti " Ndi wouma mutu Najereyu". Komatu izi si zoona. Zinthu zotsatirazi zingakuthandizeni inu makolo omwe muli ndi ana oterewa

1. Onenetsetsani kuti inuyo kholo, mukutsatira bwino zomwe mwana wanu amalemba ku sukulu. Muziona mkope mwake. Izi zidzakuthandizani kuti mudziwe zofooka za mwana wanu( Kapena kuti maphunziro omwe mwana wanu amamuvuta).

2. Onetsetsani kuti aphunzitsi a mwana wanu akhale mzanu osati mdani wanu. Pewani kumufotokozera mwana wanu zofooka za amphunzitsi akewo chifukwatu izi zingachititse mwanayo kuti asamalemekeze amphunzitsi akewo. Muzimuuza mwana wanu zabwino za amphunzitsi akewo ndipo muzimulimbikitsa kuti aziwalemekeza. Ngati mwaona kuti aphunzitsi a mwanayo alakwitsa penapake, zingakhale bwino kukambirana mwana wanuyo palibe.

3. Muzifusa aphunzitsi a mwana wanu kuti akuuzeni zomwe mwana wanu zimamuvuta mkalasi. Popeza kuti amphunzitsiwa ndi omwe amawadziwa bwino ana, angakuuzeniso njira zomwe mungatsate kuti muthandize mwana wanu.

4. Ngati simungakwanitse kumuthandiza mwana wanu panokha pemphani aphunzitsi ake kapena munthu wina waukadaulo kuti
azimuthandiza mbali zomwe zimamuvuta.

5. Ngati mwana wanu akulephera kwambiri, pewani kumuyankhula mawu ofooketsa kapena achipongwe. Mmalo mwake, muzimulimbikitsa.

Dziwani kuti, kuti mwana azichita bwino, zimadalira kuti inu makolo ndi aphunzitsi mugwirane manja.

Zabwino zonse MAKOLO
Wanuwanu Enerst M Manyoni

25/11/2023

Amalawi oposa oposa mazana awiri (200) omwe ambiri ndi achinyamata dzulo akwera ndege kuuyatsa ulendo wa ku Israel komwe boma ati lawapezera mwayi wa ntchito kumeneko.

Malingana ndi malipoti, izi zachitika potsatira kuchoka kwa nzika za dziko la Thailand zomwe zinkagwira ntchito mma famu ku Israel_ko ndipo amalawiwa azikagwira ntchito mmafamuwa.

Ngakhale kuti anthu ambiri kuno kumudzi ali ndi nkhawa kuti mwina moyo wa amalawiwa ukhoza kukhala pampeni potengera kuti paja nkhondo ya dziko la Israel ndi gulu la Hamas yomwe ili mkati, anthuwa anali achimwemwe zedi pomwe amanyamaka ulendowu pa bwalo la ndege la Kamuzu International Airport mu mzinda wa Lilongwe.

Pali chiyembekezo choti amalawiwa akakhala ku Israel nthawi yopitirira zaka zisanu
Olemba-Enest Manyoni

Address

Lilongwe

Website

Alerts

Be the first to know and let us send you an email when Matindi JourNey posts news and promotions. Your email address will not be used for any other purpose, and you can unsubscribe at any time.

Share