07/08/2026
M'modzi mwa ophunzira ku sukulu ya Bilal Darul uloom mu mzinda wa Blantyre, Abdurahim Ishmael Musah, wanyamuka m'dziko lino masana a tsiku lachinayi pa 6 August 2026 pomwe akulowera m'dziko la Saud Arabia ku mpikisano oloweza buku lolemekezeka la Quran.
Mpikisanowu omwe umakonzedwa ndi mfumu Abdul Aziz ya m'dziko la Saudi Arabia, umabweretsa pamodzi anyamata omwe analoweza buku lolemekezeka la Quran kuchokera m'maiko osiyanasiyana.
Pa mpikisano wa chaka chino omwe ukuchitika ka chi nambala 46,wabweretsa pamodzi achinyamata okwana 334 kuchokera mmaiko 133 ndipo opambana apatsidwa Ndalama zokwana SAR4 million (K1,846,599,265.60).
Polakhula za mpikisanowu, Musah wati anapeza mwayiwu pambuyo pofikira bungwe la Muslim Association of Malawi (MAM), kuti limuthandizire momwe angapezere mwayi okatenga nawo gawo ku mpikisanowu.
"bungwe la MAM, linandilembetsera ku mpikisanowu pambuyo powona zonse zoziyenereza zomwe ndili nazo, kotero zinapangitsa oyendetsa mpikisanowu m'dziko la Saudi Arabia kundivomereza,"watero M***ah.
M***ah yemwe ali ndi zaka 23 ndipo amachokera m'boma la Machinga, wati khumbo lake ndi lokachita bwino ku mpikisanowu pokapezeka malo abwino ndi cholinga choti achinyamata ena azapindule mosavuta m'mipikisano ya mtsogolo.
"ndikakhala kwa sabata ziwiri m'dziko limeneli kotero ndikupempha anthu andithandizillre ma dua ndi cholinga choti ndikachite bwino komanso ndi kapereke chithunzithunzi cha bwino cha dziko la Malawi," anaonjezelanso choncho M***ah.
M***a wakhala akutenga nawo gawo mmipikisano ingapo m'dziko muno ngati wa Malawi National Holy Quran mchaka cha 2022, pomwe anathera nambala ya chiwiri komanso mpikisano wa King Muhammad omwe anatengapo mphoto ya majuzu 20 mchaka cha 2019 komanso poloweza Quran yonse mchaka cha 2023.